MEPA House, Nkhalango Street, Lilongwe, 207213 | information@mepa.mw

Chidziwitso - Mapepala Opyapyala

Chidziwitso - Mapepala Opyapyala

Chidziwitso - Mapepala Opyapyala

Emily Phiri
Mar 17, 2026
2 min read
Updated Mar 27, 2026

Bungwe la Malawi Environment Protection Authority (MEPA) likukumbutsa anthu onse, kuti kulowetsa m’dziko, kugawa, kugulitsa kapena kugwiritsa ntchito mapepala opyapyala (omwe amadziwika kuti thin plastics) n’zoletsedwa m’dziko la Malawi malinga ndi malamulo a Environment Management (Plastics) Regulations, 2015. Komanso, mapepala opyapyala onse opanda dzina ndi nambala za omwe anawapanga, kapena opanda chizindikiro chosonyeza kuti angathe kubwezeredwanso (recyclable) n’zoletsedwa.


Pakali pano, MEPA ikuyendera ndi kuyang’anira mmisika ya mdziko lino kuti awonetsetse kuti aliyense akutsatira lamuloli. Pa ntchitoyi, mapepala opyapyala onse omwe ndi oletsedwawa akapezeka ali m’manja, m’masitolo kapena akugulitsidwa adzalandidwa, ndipo chilango chovomerezeka ndi lamulo chidzaperekedwa kwa ophwanya lamuloli. 


MEPA ikupempha amalonda onse, ogulitsa komanso ogula kuti asiye kugwiritsa ntchito mapepala opyapyala ndipo MEPA ikulimbikitsanso a Malawi kuti ayambe kugwiritsa ntchito njira zina zomwe ndi zosawononga chilengedwe monga matumba ansalu, zolukidwa, ndi zina zomwe siziononga chilengedwe. 


Anthu onse akulimbikitsidwa kuthandiza pantchitoyi pakusiya kugula ndi kugwiritsa ntchito mapepala opyapyala, komanso pakupereka malipoti ku MEPA poyimba phone yaulere pa nambala iyi 5153 pomwe mwaona anthu kapena makampani akupititsa patsogolo mchitidwe oletsedwawu. 


Kusatsatira malamulo a Plastics Regulations ndi mlandu, ndipo opezeka akutero adzalandidwa katundu wake, zida zake, kulipitsidwa chindapusa, kutsekedwa malo ogulitsira, kapena kuperekedwanso kukhoti. Bungwe la MEPA nthawi zonse limaika chidwi chake pakuteteza chilengedwe, ndi miyoyo ya a Malawi.